Kafukufuku wawonetsa kuti nkhanza zomwe ana amakumana nazo zikuchuluka m’dziko muno. Ana amakumana ndi nkhanza kunyumba, ku sukulu komanso munjira pamene akupita kapena kuchokera ku sukulu. Izi zili chomwechi chifukwa chakuti makolo komanso adindo ambiri samadziwa malamulo omwe amateteza ana ku nkhanza. Bukuli lakonzedwa ndi bungwe la Law Commission mogwirizana ndi Unicef pofuna kudziwitsa makolo komanso adindo za malamulo omwe amateteza ana ku nkhanza komanso kupereka njira zomwe makolo ndi adindo angagwiritse ntchito popewa ndi kuteteza mwana komanso kuchitapo kanthu pamene mwana wachitiridwa nkhanza. Ntchitoyi ikugwiridwa pansi pa ndondomeko ya Safe Schools Programme ndi thandizo lochokera ku Spotlight Initiative (SI) komanso United Nations Joint Programme on Girls Education (UNJPGE)
Kuthetsa Nkhanza Kwa Ana
Powered by BetterDocs