Takulandirani ku buku ili limene cholinga chake ndi kupereka upangiri wapadera kwa alangizi ophunzitsidwa mwapadera pamene akupereka uphungu kwa atsikana ndi amayi achichepere mu mabwalo okomaniramo amene adakhazikitsidwa m'madera osiyanasiyana. Bukuli lapangidwa kuchokera ku mabuku ena ophunzitsira ovomerezeka ndi boma komanso mabungwe ena monga Comprehensive Sexuality Education (CSE), Life Skills for Out of School Youth, Youth Friendly Health Services Manual and Gender Manual. Cholinga chake ndi chakuti bukuli likhale chipangizo cha alangizi chifuka mwalembedwa mfundo zambiri zofunikazimene zatengedwa kuchokera ku mabuku ena. Izi zithandiza alangizi athu kuti azigwiritsa ntchito buku limodzili m'mene muli mfundo zonse zofotokozedwa bwino m'malo momawerenga mabuku angapo pamene akuphunzitsa.
Maphunziro Osulira Atsikana m’Malo Otetezeka Mfundo Zatsatanetsatane za Aphunzitsi
Powered by BetterDocs